A Mpinganjira ndi a Ziphuphu

Thom Mpinganjira

Mpondamatiki Thom Mpinganjira wapezeka olakwa pa milandu iwiri mwa milandu isanu ndi Umodzi yokhuza kuchita upo ofuna kupereka ziphuphu kwa oweruza asanu omwe amanva mlandu wa chisankho cha mtsogoleri cha mu 2019.

Bungwe la ACB linatengera ku bwalolo a Mpinganjira, oweluzawa atakamang’ala ku bungweli ponena kuti mkuluyu amafuna kuwakopa kuti akondere mbali ya odandaulidwa pa mlanduwo omwe anali mtsogoleri wakale wa dziko lino, Peter Mutharika mu chigamulo chawo.

Popereka chigamulo chake, oweruza Dorothy DeGabriele anati umboni omwe unaperekedwa ndi mbali ya ACB unatsimikizira kuti mkuluyu analidi ndi upo ofuna kuchita za katangale.

Oweruzayu watinso pa nthawi yomwe mkuluyu amayankha mafunso kwa ma-lawyer, anavomereza kuti analidi ndi malingaliro otero.

Pakadali pano, bwalo lachotsa bail ya a Mpinganjira ndipo akuwasunga ku ndende ya Chichiri kudikira chigamulo.

Poyankhapo pakupezeka kulakwa kwawo, Lawyer wawo, Tamanda Chokhoto anapempha oweruza Dorothy DeGabrielle kuti aganizire zopereka chilango chofewa kwa a Mpinganjira poa nthawo yomwe bwalo lizizawagamula.

A Chokhoto mwa zina ati mkuluyu ndi munthu wabwino, uku ndi kupalamula kwake koyamba,amathandiza timu ya mpira wa miyendo ya Mighty Wanderers, ali ndi zaka 60 komanso anayambitsa bank ya FDH choncho sakuyenera chilango chokhwima.

Reyneck Matemba

Koma yemwe amaimira ACB pa mlanduwu, Reyneck Matemba poyankhula ndi atolankhani anati mfundo za a Chokhoto ndi zosamveka popereka chitsanzo choti bank ya FDH ili ndi utsogoleri wakewake komanso kuti a Mpinganjira akanayamba alingalira asanapalamule milanduyi.

Otsatira Mpinganjira Kusonkhana Panja pa Bwalo la Milandu

Kunja kwa bwalolo kunali chitetezo pomwe anthu ena omwe anavala zovala zaonetsa nkhope ya a Thom Mpinganjira anasonkhana ndi kumaimba nyimbo zotamanda mkuluyu.

Gallery for A Mpinganjira ndi a Ziphuphu

Please follow and like us:
Pin Share
(Visited 108 times, 1 visits today)

RSS
Follow by Email