Chakwera Anaphwanya Malamulo-Court

Lazarus Chakwera

Bwalo la High Court lati President Lazarus Chakwera anaphwanya malamulo pobwezeletsa pa mpando Noah Dalasi ngati mfumu yaikulu Ngabu ya m’boma la Chikwawa.

Oweruza mlandu Justice Mandala Mambulatsa ndi yemwe wapereka chigamulochi la Chiwiri ponena kuti kubwezeletsedwa kwa a Dalasi kunali kotsatsata malamulo a dziko lino.

Justice Mandala Mambulatsa walamulanso President Lazarus Chakwera apereke ndalama zonse zomwe zagwiritsidwa ndi mbali yodandaula pa mlandu-u, zomwe ndikuphatikiza zolipilira ma lawyer.

Chigamulochi chaperekedwa bambo Basitole Dalison Makwalu, omwe anasankhidwanso kuti alowe m’malo mwa mfumu Yaikulu Ngabu atakamang’ara ku bwalo kutsatira kubwezeretsedwa pa Mpando kwa a Dalasi ndi President Chakwera.

A Dalasi anachotsedwa ngati mfumu yaikulu Ngabu pa 12 December 2019 ndi yemwe anali President wa dziko lino a Peter Mutharika, poyiganizira kuti imakhuzidwa ndi nkhani za katangale.

Gallery for Chakwera Anaphwanya Malamulo-Court

Please follow and like us:
Pin Share
(Visited 159 times, 1 visits today)

RSS
Follow by Email