Robert Mugabe Aikidwanso M’manda

Robert Mugabe

Bwalo la milandu m’dziko la Zimbabwe lagwirizana ndi chigamulo cha mfumu Zvimba ya kumeneko choti thupi la mtsogoleri wakale wa dzikoli, Robert Mugabe alifukule ndipo liikidwenso m’maso.

Mfumu Zvimba inati thupili silinaikidwe m’manda mwa Ulemu wake komanso linaikidwa ku manda a banja koma mwa ndondomeko yake, limayenera kukaikidwa ku manda omwe anthu olemekezeka amaikidwa.

Komatu ana a malemu Robert Mugabe anatsutsana ndi chigamulochi chomwenso chinapeza mkazi wa malemu-yu, Grace Mugabe olakwa potsogolera kuti thupili liikidwe m’manda mosasata ndondomeko.

Malingana ndi ana-wa, malemu Mugabe anachita kusankha asanamwalire kuti azaikidwe ku manda a ku banja ndi cholinga choti mtsogoleri wa dzikoli, Emmerson Mnangagwa asazakhale nawo pa mwambo omuika m’manda.

Komatu nkhaniyi ataitengera ku bwalo la milandu, oweruza anati palibe cholakwika chomwe mfumu Zvimba anachita polamula kuti thupili lifukulidwe ndi kuikidwanso m’manda mosata ndondomeko.

Robert Mugabe anamwalira mchaka cha 2019 ali ndi zaka 95 ndipo atamwalira, panali kukokana kwakulu pakati pa boma ndi a ku banja pa za komwe thupili liikidwe m’manda kufikira linakaikidwa ku mudzi kwawo.

Gallery for Robert Mugabe Aikidwanso M’manda

Please follow and like us:
Pin Share
(Visited 130 times, 1 visits today)

RSS
Follow by Email