Mnyamata wina ku Chilomoni ali ku chipatala komwe akulandira thandizo la mankhwala, mnzake wina atamumenya ndi mpini ati kaamba koti amafuna kudya nawo nsima ya m’memo omwe sanasonkhe.
Yemwe watitumizira nkhani-yi wati monga mwa nthawi zonse amnayamatawa asonkha ndalama ya m’memo wa tsikuli koma m’modzi mwa iwo sanasonkhe ngakhale pa nthawi ya kudya anali liki-liki kufuna kudya nawo zomwe zinakwiyitsa m’modzi mwa omwe anasonkha m’memowu.
Apa kulimbana kunabuka komwe cholinga chake chinali choti mkuluyu asadye koma iye amachita makani ponena kuti adya.
Kulimbanaku kutakula, mkulu osasonkhayu anangozindikira mpini uli m’mutu mpaka thapsa.
Pakadali pano, malipoti akuti mkulu yemwe wachita za upanduzi wathawa ndipo apolisi akumusaka-saka pomwe osasonkhayu ali mchipatala komwe akulandira thandizo.